Bungwe la utumiki wa a Papa mdziko muno la Pontifical Mission Socities PMS lati asemino akuyenera kukhala patsogolo kudziwa zomwe bungwe la utumiki wa apapa limachita.
Mkulu wa bungweli mdziko muno Bambo Vincent Mwakhwawa ndi omwe alankhula izi pambuyo pa maphunziro a masiku asanu omwe bungweli linakonzera asemino omwe akuphunzira ku seminale yaikulu ya St. Peter’s mu dayosizi ya Zomba.
Iwo ati pozindikira kuti iwo ndi omwe amakhala ndi anthu m’madera osiyanasiyana, ali ndi kuthekera kothandiza anthu za cholinga cha bungweli.
Polankhulapo m’malo mwa ophunzira a pa seminaleyi, Deacon Paul Mkumbira wati wapindula ndi maphunzirowa kaamba koti adziwa njira zabwino zomwe adzagwiritse ntchito pochita utumiki wao.