Ma episkopi a mpingo wa katolika m’dziko la Nigeria apempha atsogoleri a dzikolo kuti ayesetse kuteteza ufulu wa anthu m’dzikomo.
Malingana ndi malipoti a Catholic News Agencyma episkopiwa alankhula izi atachita zokambilana masiwa apitawa.
Iwo ati dzikolo likukumana ndi mavuto osiyanasiyana monga a umphawi ndi za mtopola zomwe gulu la zauchifwamba la Boko Haramu ndi magulu ena a zauchifwamba akulimbikitsa m’dzikomo.
Iwo alangiza mzika za dzikolo kuti zikhale zogwirizana pofuna kuthana ndi mavutowa.