Loya wina yemwe amayimilira munthu wina pamlandu woti apolisi m`dziko la Kenyaakumachitira nkhanza anthu m`dzikolo wapezeka atafa munzinda wa Nairobi m`dzikolo.
Loyayu, Willie Kimani wa zaka 32, pamodzi ndi dalaivala yemwe amamuyendetsa pathawiyo anasowa sabata yapitayo atangotuluka mu bwalo la milandu. Thupi la mkuluyu ati alipeza litakulungidwa m`phepete mwa mtsinje wina omwe uli pamtunda wa makilomita 70 kumwera chakum`mawa kwa mzinda wa Nairobi.
Bungwe la Malamulo m`dzikolo lati kuphedwa kwa loyayu ndi chinthu chomvetsa chisoni kwambiri pantchito yoteteza malamulo a dzikolo.
Apolisi mdziko la Kenya akhala akudzudzulidwa kuti amachitira nkhanza mzika zadzikolo komanso kugwirizana ndi mbava polimbikitsa umbanda ndi umbava.
Pakadali pano mkulu wa apolisi mdzikolo walamula kuti apolisi atatu amene akuganiziridwa kuti ndi amene achita izi amangidwe.