Ofesi yoona za umoyo m’boma la Rumphi yapempha adindo a m’bomalo kuti awonetsetse kuti ana 95 mwa 1 hundred aliwonse oyambira miyezi 9 mpaka zaka 14 alandire katemera wa matenda a chikuku.
Mmodzi mwa akuluakulu ku ofesiyi mayi Patricia Mweso ndi omwe alankhula izi pa msonkhano omwe anali nawo ndi komiti ya bomali wokambira za dongosolo la ntchito yopereka katemerayu.
Iwo apempha adindo omwe akukhudzidwa ndi ntchitoyi kuti azipereka uthenga wolondora kwa anthu kamba koti ena amakhala ndi chinthunzinthunzi chosayenera pa nkhani ya katemerayu kaamba ka zikhulupiliro zomwe ali nazo.
Mayi Mweso ati unduna wa za umoyo wapeza anthu ochokera ku nthambi zosiyanasiyana za boma ngakhalenso ku mabungwe omwe si a boma kuti awuthandize kufikira ana omwe ali m’madera ovuta kufikira.
Boma la Rumphi likuyembekezeka kupereka katemera wa chikuku kwa ana oposera 1 hundred sauzande.