Bungwe la Worldfish Centre lati tsopano ligwira ntchito ndi atolankhani pofalitsa uthenga wa zotsatira zakafukufuku yemwe bungweli limachita wokhudza ulimi komanso usodzi wa nsomba.
Mkulu wa bungweli mdziko muno aJoseph Nagolialankhula izi pa msonkhano omwe bungweli linakonzera atolankhani mu mzinda wa Zomba.
Iwo ati kafukufuku yemwe bungweli lakhala likuchita sanapindulire anthu ambiri mdziko muno kamba koti zotsatira zake zimalembedwa mziyankhulo zomwe anthu akumidzi sakanatha kulandira uthengawu ndi kuwugwilitsa ntchito, ndipo ndi chifukwa chake awona kuti nkofunika kugwira ntchito ndi atolankhani omwe angathe kufotokozera bwino anthu zotsatira zomwe bungweli lapeza kuti ziwapindulire.
Bungwe la Worldfish Centre linayamba kugwira ntchito zake mdziko muno mchaka cha 1987 ndipo cholinga cha kafukufukuyu ndi kufuna kuchepetsa njala ndi matenda onyetchera mdziko muno.