Mnyamata wina wa zaka 14 zakubadwa wafa ng’ona itamugwira pa doko la Kambulire pa nyanja ya Malombe m’boma la Mangochi.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Inspector Rodrick Maida watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati mnyamatayo Edson Asima yemwe amakhala mmudzi mwa Kambulire kwa mfumu yaikulu Chimwala m’bomalo, pa tsikulo malinga ndi mai ake Isha Wyson, malemuyu ndi anzake anapita ku dokoli komwe amakasambila ndipo ng’onayo inamugwira pa nthawi imene anali kusambila pa malowo.
Inspector Maida ati anthu a mmudziwo anafunafuna mnyamatayu ndipo pa nthawi yomwe amamupeza anali atafa kale.
Malipoti ochokera kuchipatala chaching’ono cha Lukalanga asonyeza kuti Edson wamwalira kaamba kobanika komanso kutaya magazi ochuluka.