Mpingo wa Anglican m’boma la Kasungu wapempha anthu akufuna kwabwino kuti athandize malo osamalirako ana amasiye ndi ovutika omwe mpingowu uli nawo ku Nthunthama m’bomalo.
Mpingowu wati ukusowa thandizo la ndalama ndi katundu wina wothandizira ana amasiye ndi ovutika omwe umawasamalira ku malowa.
Iwo ati mwa zina thandizolo ndi oti agulire zinthu zina monga chakudya komanso ndalama zokalipilira sukulu ana amene afika pa mulingo wokachita maphunziro awo ku sukulu za pa mwamba.
Malingana ndi wapampando wa ku malo opelekera chisamaliro cha anawa omwe ali ku tchalichi la mpingowu la All Saints ku Ntunthama a Nelson Japan ati padakalipano mpingowu ukupeleka chisamaliro kwa ana okwana 114 omwe ambiri mwa iwo ndi oti anayamba kulandira chisamaliro pa malowa adakali akhanda ndipo ndi ochokera m’ma boma a Kasungu ndi Ntchisi.
Malingana ndi malipoti a Malawi News Agency-MANA,padakalipano bank yaNational ndi yomwe yawonetsapo chidwi chothandiza malowa ndi katundu wina monga belo la zovala, sugar, sopo, mafuta odzola ndi ufa wa Phala la Likuni.