Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Azikanena Ku Khonsolo Akachitiridwa Nkhanza

$
0
0

Khosolo ya mzinda wa Blantyre yapempha anthu malonda mu mzindawu kuti azikanena ku khosoloyi pa nkhanza zina zili zonse zomwe angachitiridwe ndi anthu ogwira ntchito kukhosoloyi.

Wofalitsa nkhani ku khosoloyi a Anthony Kasunda anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi pomwe amafuna kudziwa zomwe khosoloyi ikuchita pofuna kuthana ndi nkhanza zomwe ogwira ntchito ku khosoloyi akumachitira anthu ochita malonda mu mzindawu.

Izi zili chonchi potsatira kuchuluka kwa madandaulo omwe ochita malonda-wa mu mzindawu akumakhala nawo  okhudza ogwira ntchito kukhosolo-yi.

“Khonsolo yathu ndi yomasuka kwambiri kulandira chidandaulo chilichonse. koma anthu azindikire kuti khonsolo ya Blantyre silora kuchita malonda munsewu koma munsika. anthuwa pamene tikuwalanda katundu sasangalala ayi chonchi amatha kumenya munthu wathu,” anatero a kasunda.

A Kasunda apempha anthu omwe amachita malonda m’misewu ya munzindawu kuti akayambe kugulitsa zinthu zawo munsika kuti apewe kulandidwa katundu wawo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>