Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mwambo Wopereka Ma Degree ku ICI

$
0
0

Mwambo wopereka ma degree kwa ophunzira omwe amaliza maphunziro awo a Philosophy ku  International Congregation Institute (ICI) m’boma la Balaka wachitika loweluka pa 3 June  Chaka chino.

Mmawu awo mlendo wolemekezeka ku mwambowu Ambuye Martin Mtumbuka omweso ndi wapampando wa sukulu za ukachenjede za mpingo wakatolika mdziko muno, anapempha Ophunzirawa kuti akapitirize kukhala a makhalidwe abwino komanso chitsanzo kwa anthu ena. Mwa zina Ambuye Mtumbuka apempha ophunzirawa kuti akakhale anthu okonda dziko lawo popewa katangale ndi ziphuphu komanso kukonda kulimbika kugwira ntchito. Ophunzira pafupifupi 33 ndi amwe amaliza maphunziro awo a philosophy pa sukuluyi ndipo akuchokera mzipani zosiyanasiyana za mu mpingo wakatolika mmaiko amuno mu Africa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>