Apolisi m’boma la Nsanje akusunga m’chitolokosi amuna awiri kaamba kowaganizira kuti anapha Njati mu nkhalango ya boma ya Mwamvi Game Reserve.
Ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sargent Agnesi Zalakoma wauza atolankhani a Malawi News Agency (MANA) kuti a Ruo Khambaza a zaka 24 zakubadwa ndi a Jailosi Fungulani a zaka 48 zakubadwa adapha Njati-yi zomwe ati ndizosemphana ndi malamulo oyendetsera dziko lino . amuna-wa ndi a m’mudzi mwa mpangira m’boma lomweli la Nsanje ndipo akaonekera ku khoti kukayankha milandu yawo posachedwapa.