Anthu anayi afa ndipo ena avulala modetsa nkhawa pa ngozi ya galimoto zomwe zinaombana m’boma la Dowa.
Malinga ndi ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergent Richard Kaponda ngoziyi yachitikira pafupi ndi msika wa Chankhungu m’bomalo ndipo mwa anthu anayi omwe amwalirawo atatu ndi a Pilirani Lenard, Lupiya Michael komanso Junior Chiunjika ndipo onsewa amachokera pa msika wa Bowe kwa mfumu yaikulu Chakhadza m’boma lomwelo la Dowa ndipo m’modziyu sanadziwikebe komwe amachokera.
Galimotozi ndi za mtundu wa Toyota Hilux zomwe zimayendetsedwa ndi a Lucious Yohane komanso a William Phiri, ina imachokera mbali ya Salima kupita ku Lilongwe pomwe ina imachokera ku Lilongwe kupita ku Salima ndipo ngozi-yi yachitika pomwe ma dalaivala awiriwa analephera kuwongolera.
Anthu ovulalawa anawatengera ku chipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe komwe akulandira thandizo ndipo matupi a omwalirawa akuwasunga ku nyumba ya chisoni ya chipatala chachikulu cha Dowa.