Apolisi ku Kanengo mu m’zinda wa Lilongwe akusunga m’chitolokosi bambo wina wa dzaka 36 zakubadwa kamba komuganizira kuti anamenya ndikupha mkazi wake.
Ofalitsa nkhani za apolisi ku delaro Sergeant Salome Zgambo Chibwana watsimikzira za nkhani-yi ndipo wati bamboyu ndi Major Willson ndipo anamenya Teleza Namizinga Willson a zaka 32 zakubadwwa kaamba kowaganizira kuti amachita chibwenzi cha mseli ndi mwamuna wina.
Bamboyu akuti anachitira za upandu mkazi wakeyu pa 2 mwezi omwe uno pomwenso anthu ena akufuna kwabwwino anatengera kuchipatala cha Kamuzu Central komwe anatsimikidza kuti malemuyi anali atamwalira kaamba koti anataya magazi ambiri.
A Major Willson amachokera m’mudzi mwa m’denga kwa mfumu yaikulu Nsamala m’boma la Balaka pamene malemumkazi wawoyu amachokera m’mudzi mwa Namate m’dera la mfumu yaikulu Mthiramanja m’boma la Mulanje.
Ndipo pakadali pano a Major Willson akuyembekedzeka kukaonekera ku khothi ndikukayankha mlandu wawo.