M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco amuyamikira kamba kothilirapo ndemanga ponena kuti chipembedzo cha chisilamu si chofanana ndi magulu omwe amakhala akuchita za uchifwamba.
Mkulu wa chipembedzochi m’dziko la Iran, a Ayatolla Makarem Shirazi walankhula izi kudzera mu kalata yomwe walemba pa tsamba lake la pa makina a Intaneti.
A Shirazi ati akugwilizana ndi mau omwe m’tsogoleri wa mpingo wakatolikayu analankhula kuti zauchifwamba zomwe zikuchitika m’maiko osiyanasiyana sizichokera mu chipembedzo cha chisilamu.
Pamenepa a Shiraz anati apitiriza kumupemphelera Papa Francisco kuti apitirize kutumikira Mulungu.