Ofesi yoona za umoyo m’boma la Mangochi yapempha amayi kuti akayezetse khansa ya khomo la chiberekero ndi cholinga choti adziwe ngati ali ndi vutoli kapena ayi.
Dotolo wa mkulu m’bomali Dr Henery Chibowa ndi yemwe wanena izi pa mwambo wolandira thandizo la makina othandizira pa ntchito zina za umoyo kuchokera ku bungweli la Saint Egidio lomwe ndi lopezeka mu mpingo wakatolika.
Dr Chibowa ati mwa amayi 1000 omwe anayezedwa matendawa ndi amayi 300 omwe awonetsa zizindikiro za matendawa ndipo amayi 40 ndi omwe apezeka kuti ali ndi khansa ya mtundu-wu.
Iwo ati zomwe azaumoyowa apeza zikusonyeza kuti vuto la matendwa litha kukhala lalikulu pakati pa amyi mbomalo potengelanso kuti amayi ambiri sakuonetsa chidwi chofuna kudziwa za miyoyo yawo pankhani zokhudza matendawa.
Pamenepa iwo alangiza amayi onse a m’bomali kuti asanyozere koma kuti akayezetse ndi kuti ngati atapezeka ndi zizindikiro kapena matenda-wa athandizidwe mwa msanga.
Polankhulanso mkulu woyendetsa ntchito za chipatala cha Dream m’bungwe la Saint Egidio a Lawrence Alumando anati bungwe lawo lipitiliza kuthandiza pa ntchito za umoyo m’bomalo.
Makina omwe bungwe-li lapeleka m’bomalo ndi a ndalama zokwanira 5 million kwacha.