Bungwe la Catholic Commission for Justice and Peace [CCJP] lomwe ndi nthambi ya bungwe la ma episkopi ampingo wakatolika kuno ku Malawi lapempha bungwe loona za chisankho la Malawi Electoral Commission [MEC] kuti likhwimitse malamulo ake pofuna kuti atsogoleri opezeka akukolezera ziwawa asazayime nawo pa chisankho cha pa 20 May.
Muchikalata chomwe chasainidwa ndi mlembi wamkulu wa bungwe la CCJP a Chris Chisoni bungweli ladzudzula mchitidwe wa zipolowezi za kwa Goliati mboma la Thyolo pomwe anthu awiri kuphatikizapo wapolisi ataya miyoyo yawo komanso kuvulazidwa kwa mmodzi mwa otsutsa boma mumzinda wa Blantyre lolemba.
”Tikupempha atsogoleri a zipani zonse kuti athetse mchitidwe wa ziwawa m’misonkhano yawo ndi kuthandiza owatsatira kuti akhale amtendere. Tikupemphanso bungwe loona zachisankho kuti lipeze njira zolangira zipani zomwe ziziyambitsa zisokonezo ngakhale kuchotsa atsogoleri azipani ngati zitazindikirika kuti anthu awo ndiomwe akuchita zisokonezo m’misonkhano”chatero chikalatacho.
Malinga ndi chikalatachi, chipani chili chonse mdziko muno chili ndi ufulu ochititsa misonkhano dera lili lonse ndipo kuti palibe chifukwa choti kusemphana pakayankhulidwe pakati pa zipani za ndale kuzichititsa ziwawa mmisonkhano ya ndale.
Bungweli lakumbutsa mzika za dziko lino kuti malamulo adziko lino amalola zipani zambiri zomwe zilibe malo akeake oti zizichitira misonkhano yake. Bungweli lati mchitidwe waziwawawu walikumbutsa dziko lino momwe linatayira munthu mmodzi pa mikangano ya chipani cha National Democratic Alliance NDA mchaka cha 1999 komanso miyoyo yomwe inatayika pa zionetsero zomwe mabungwe omwe si aboma anakonza pa 20 July mchaka cha 2011.
Chikalatachi chadzudzulanso mchitidwe ogwiritsa ntchito achinyamata m’misonkhano yandale kuti azichita zosokoneza momwe zachitikira ku nsonkhano wa kwa Goliatiwu. Mabungwe komanso zipembezo kuthatikizapo mpingo wa CCAP wadzudzulanso mchitidwewu.