Episikopi wa Mpingo wakatolika mu Dayosizi ya Zomba Olemekezeka Ambuye George Desmond Tambala wapempha Akhristu aku Tchalitchi cha Matawale chomwenso ati posachedwapa akufuna kuchikhadzikitsa kukhala Parish mu Dayosizi-yi kuti akhale odzidalira.
Ambuye Tambala anena idzi Lamulungu lapitali pambuyo pa mwambo wa nsembe ya Ukaristia pomwe anapita kukayendera akhristu a tcharichiri. Ambuye Tambala athokozanso akhristu a ku Matawale chifukwa chomanga nyumba yamakono komanso yaikulu yopemphereramo. Iwo ati izi zawapatsa chilimbikitso kuti mtsogolomu akhala akukhadzikitsa tchalichiri kukhala parish ndipo ati udzakhala mpingo odzidalira pawokha pazachuma.