Mfumu yayikulu ya mtundu wa Alhomwe mdziko muno yapempha ndikulangiza mafumu a mtunduwu kuti alimbikitse kusunga chikhalidwe chomwe ndi maziko a chikondi pakati pawo.
Paramount Chief Ngolongoliwa ndiwomwe alankhula izi pamene amakumana ndi mafumu ang’ono ang’ono a mtunduwu ochokera mboma la Zomba.
Ngolongoliwa wati ngati mafumu atalimbikitsa chikondi pakati pa anthu awo zingathandize kupititsa pa tsongolo ntchito za chitukuko mmadera awo.