Ngozi za pansewu m’dziko muno akuti zachepa ndi 39 percent m’miyezi isanu ndi inayi 9 yapitayi poyerekeza ndi nthawi ngati yomweyi chaka chatha.
Wofalitsa nkhani za apolisi mdziko muno a James Kadadzera anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi. Iwo ati chaka chatha kunachitika ngozi zapansewu zoposa 2 sauzande pamene chaka chino kwachitika ngozi zoposa 1sauzande.
A Kadadzera ati ngozi zachepa chotere kaamba ka ntchito yotamandika imene apolisi a pansewu mdziko muno akugwira yomanga onse ophwanya malamulo a pansewu zomwe zikuchititsa kuti madalaivala ambiri azitsatira malamulo a pansewu.