M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wafunila zabwino ma episikopi a mpingo wakatolika ochokera m’mayiko a ku ulaya la Council Of European Bishops' Conferences , omwe ali mkati kuchita msonkhano wawo m’chigawo-cho.
M’tsogoleri wa mpingo wakatolika-yu, Papa Francisco, watumiza uthenga-wu kudzera kwa mlembi wamkulu ku Vatican , Cardinal Pietro Parolin.
Mu uthanga-wo , Papa Francisco wapempha ma episikopi-wa kuti adzipereke pokambilana mfundo zothandiza pa chitukuko cha achinyamata ndi mpingo-wu m’mayikowo.