Akhristu a mpingo wakatolika mu dayosizi ya Zomba awayamikira kamba kokhadzikitsa mulozo wa mapulani a ntchito zoyendetsera parishiyo.
Episikopi wa mpingo wakatolika mu dayosizi ya Zomba olemekezeka ambuye George Desmond Tambala , ndiomwe anena izi ku parish ya St Charles Luanga mu dayosizi-yi pambuyo pa mwambo wokhadzikitsa mlozo wa momwe parishi-yo igwilire ntchito zake , mu zaka zisanu zikubwerazi.
Iwo ayamikira akhristu a mparishiyi kamba kobwelanso ndi ganizo lokhadzikitsa mapulani a zakayendetsedwe ka parishiyo mogwilizana ndi mulozo wa dayosiziyo kamba koti izi zithandiza kuti ntchito zotukula dayosiziyi zipitilire kuyenda bwino.
Polankhulanso ndi moderator a parish-yi a Robins Chiwaya ati parish yawo ikufunitsitsa kuti ikhale parish yachitsanzo polimbika pa ntchito zokweza mpingowu mu dayosiziyo ndipo chiyambi chofuna kukwanilitsa izi ndi kukhadzikitsidwa kwa mulozowo.
Mulozo umene parish ya St Charles Luanga yakhadzikitsa ndi wa zaka zisanu ndipo uli ndi mapulani antchito zosiyanasiyana zomwe zithandize pa chitukuko cha parishiyo mu dayosiziyo.