Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

BAMBO CHIWANDA ALOWA M’MANDA

$
0
0

Ma episkopi atatu ampingo wakatolika kuno ku Malawi lachinayi pa 20 march anatsogolera anthu zikwizikwi pa mwambo woyika m’manda thupi la bambo Matthias Chiwanda amu dayosizi ya Chikwawa omwe anamwalira pa 17 march atadwala kwa nthawi yochepa.

Episkopi wadayosizi ya Chikwawa Ambuye Peter Musikuwa, episkopi wadayosizi ya Mangochi Ambuye Montfort Sitima kuzanso wolemekezeka Ambuye Thomas Msusa omwe ndi arki episkopi wa arki dayosizi ya Blantyre ndi omwe anali nawo pa mwambowo ku seminare ya Mzimu Woyera ku Chikwawa.

Polankhula pamene anatsogolera mwambo wa msembe ya misa ya maliro ku St Micheals Cathedral Ambuye Musikuwa, anati amsembe ndi ofunikira kwambiri kamba koti ndi omwe amapereka masacramenti kwa akhristu ndipo anati imfa ya bamboo Chiwanda ndi yodandaulitsa ku mpingo onse.

“Ndine okhumudwa kwambiri ndi imfa imeneyi. Amsembe ndi omwe amatithandiza ife ma episkopi poyendetsa maparishi m’malo mwathu komanso kupereka ma sacramenti kwa akhristu. Imfa ya bambo Chiwanda ndi chiphinjo kwa ine, mpingo onse kuno ku Chikwawa ngakhalenso mumpingo wathu.” Anatero Ambuye Musikuwa.

Mu kulira kwawo, Bambo Benedict Liyao omwe ndi membala wakomiti ya bungwe la amsembe achibadwiri kuno ku Malawi la Association of Diocesan Catholic Clergy of Malawi (ADCCOM), lomwe wapampando wake anali malemu bambo Chiwanda, anati mpingo wa katolika kuno ku Malawi unadzidzimuka utamva za imfa ya bamboo Chiwanda.

Bambo Liyao anatsimikizira amsembe onse mu bungweli kuti Mulungu yekha ndi yemwe ali ndi mayankho ndipo ndi Mulungu yemweyo yemwe atsogolere bungwelo ngakhalenso dayosizi ya Chikwawa popereka mlowa m’malo wawo.

Ena mwa anthu omwe anafika pa mwambowo ndi nduna ya migodi a John Bande, a Harry Thomson, mlembi wamkulu wabungwe la Episcopal Conference of Malawi ECM Bambo George Buleya komanso amsembe ochuluka ochokera mma dayosizi onse kuno ku Malawi.

Bambo Chiwanda omwe amwalilira pachipatala cha Kalemba mboma la Nsanje anabadwa pa 12 July mchaka 1969 ndipo amachokera m’mudzi mwa Sorgin mfumu yaikulu Mbenje m’Parishi ya Bangula mboma la Chikwawa.

Malemuwa anazozedwa unsembe pa 16 July mchaka 1995 ku Chikwawa Cathedral ndipo atumikirapo m’ma Parishi a Nsanje, Misomali, Ngabu kuphatikizaponso ndi ku Nsanje Spirituality Centre komanso kusukulu ya asemino ya Mzimu Woyera.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>