Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bambo Wina Amunjata Kamba Komuganizira Kuti Wapha Mkazi Wake.

$
0
0

Apolisi m’boma la Mangochi akusunga m’chitokosi bambo wina amene akumuganizira kuti wapha mkazi wake .

Malingana ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergent Amina Tepani Daudi bamboyu ndi Saizi Kanjinga wa zaka 48 zakubawa amene amachokera m’mudzi mwa Fundi m’dera la mfumu yayikulu Mponda m’bomalo.

Sergent Tepani wati bamboyu anapalamula mulanduwu pa 3 September 2017 atamenya ndi kuvulaza mkazi wakeyu amene anakamwalira ku chipatala.

Padakalipano a Saizi Kanjira akaonekera ku bwalo la milandu posachedwapa. 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>