Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Antchito a Mtsogoleri wa Dziko la South Korea Amangidwa

$
0
0

Apolisi otengera nkhani ku bwalo la milandu mdziko la South Korea apereka chilolezo kuti apolisi amange antchito awiri a mtsogoleri wa dzikolo ngati mbali imodzi yofufuza katangale amene akuchitika mdzikolo.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, mtsogoleri wa dzikolo komanso akuluakulu ena a boma akukhudzidwa ndi katangale komanso kugwiritsa ntchito udindo wawo molakwika.

Padakali pano mtsogoleriyu akuti wapepesa kudzera pa wailesi ya kanema ya dzikolo koma chipani chachikulu chotsutsa boma cha dzikolo chati kupepesaku kunasowa chilungamo ndipo mtsogoleriyu akuyenera kuchoka pa udindowu.

Anthu mazanamazana a dzikolo akhala akuchita chionetsero ku likulu kwa dzikolo ku Seoul kuti mtsogoleriyu atule pansi udindo wake koma iye wakanitsitsa kuti sangatule pansi udindo wake.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>