Bungwe la mgwirizano wa maiko a mu Africa la African Union (AU), lati zomwe achita asilikali a dziko la Zimbabwe potenga udindo oyendetsa boma, ndi chimodzimodzi kulanda boma ngakhale asilikaliwo akutsutsa izi.
Wapampando wa bungweli a Alpha Conde, yemwenso ndi mtsogoleri wadziko la Guinea, ndi yemwe wanena izi, ndipo walamula kuti zonse zibwelere mchimake pofuna kulemekeza malamulo akayendetsedwe ka boma mdzikolo.
Asilikaliwo akukanitsitsa kuti iwo sadalande boma koma akufuna kuthana ndi anthu omwe akulimbirana maudindo mchipani cholamula cha ZANU-PF, pamene anthu mdzikolo ali pa mavuto aakulu a zachuma.
Masiku apitawa, pulezidenti Mugabe wachotsa paudindo wachiwiri wake a Emmerson Mnangagwa zomwe malinga ndi malipoti a BBC, zingathe kupereka mpata kwa mai wa fuko la dzikolo Grace Mugabe, yemwenso akufuna udindo wa pulezidenti, kuti atenge udindowu mosavuta.
Malipoti ena akusonyeza kuti pamene a Mugabe akusungidwa mokakamiza ndi asilikaliwo mkazi wawo Grace Mugabe, wathawira mdzilo la Namibia.
Lachitatu a Mugabe akuti adaimbira lamya mtsogoleri wa dziko la South Africa Jacob Zuma kumufotokozera kuti ali bwino.
Dziko la Egypt lidachotsedwa m’bungwe la African Union, magulu owukira atalanda boma mchaka cha 2013, zomwenso akuti zingathe kuchitikira dziko la Zimbabwe ngati ulamulirowo, ungapitilire kukhala m’manja mwa asilikali.