Bwalo loyamba la milandu m’boma la Machinga lalamula mzimayi wina wa zaka 26 zakubadwa kuti akakhale kundende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka zitatu kaamba kopezeka olakwa pa mlandu wochita za dama ndi m’nyamata wina wopemphapempha m’bomalo.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Constable Davie Sulumba watsimikiza izi ndipo wati bwaloli kudzera mwa wapolisi wotengera nkhani ku bwalo la milandu Sergeant Joel Kabichi linamva kuti pa 28 mwezi watha mayiyu Iness Salamba anayitana m’nyamatayu Gift Afiya yemwenso amadwala nthenda ya khunyu, kunyumba kwake komwe anakachita naye zadama.
Mayi ake a mnyamatayu atamuona ati anadabwa ndi mmene amawonekera ndipo atamufunsa ndi pomwe amafotokoza za nkhaniyi pambuyo pake mayiyo ati anatengera nkhaniyi kwa a mfumu omwe anakanena nkhaniyi ku polisi.
Mayiyu atapezeka olakwa Sergeant Kabichi anapempha bwaloli kuti lipereke chilango chokhwima potengera chilango chomwe amapereka kwa munthu wam’muna akagwililira munthu wamkazi.
Asanalandire chigamulo mayi Iness anapempha bwaloli kuti limuganizire kaamba koti ali ndi mwana wa Fomu 2 yemwe amadalira thandizo lake komanso amasamalira mwana wamasiye.
Popereka chigamulo chake oweruza milandu mai Esther Phiri anagwirizana ndi zomwe a mbali ya boma anadandaula ndipo ndi pomwe amapereka chigamulo cha mtunduwu.
Mai InessSalamba amachokera m’mudzi mwa Lodesi kwa mfumu yaikulu Kawinga m’boma lomwelo la Machinga.