Episkopi wa dayosizi ya Zombaya mpingo wa Katolika ambuye George Desmond Tambala loweruka likudzali akuyembekezeka kudzakhazikitsa tchalitchi la Matawale yomwe ndi nthambi ya St. Charles Lwanga kukhala parishi.
Ambuye Tambala awuza Radio Maria Malawi, kuti amene adzitumikira pa parishi yatsopanoyi ndi ansembe a chipani cha Mabala Oyera a Ambuye yesu khristu.
Iwo apempha akhristu a pa parishi yatsopanoyi, kuti adzakhale odzidalira kaamba koti masiku ano, mpingo ukuyendetsedwa ndi akhristu eni ake.
Mmawu ake mkhala pakati wa parishi yaSt. Charles Lwangayomwe yatulutsa parishi yatsopanoyi aRobins Chiwaya, ati zonse zokonzekera kukhazikitsidwa kwa parishi yatsopanoyi zikuyenda bwino.