Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anjatidwa Zaka 7 Kamba Kozembetsa Anthu

$
0
0

Bwalo loyamba la milandu m’boma la Mwanza lalamula a Elias Jafali a zaka 24 zakubadwa kuti akakhale ku ndende ndi kukagwira ntchito yakalavula gaga kwa zaka zisanu ndi ziwiri, 7 kaamba kopezeka olakwa pa mulandu wozembetsa anthu.

Bwaloli linamva kuti a Elias Jafali, anagwidwa pa 4 October 2017 pa chipata cholowera ndi kutulukira mdziko muno cha Mwanza, ali ndi anthu khumi ndi awiri 12 omwe amapita nawo ku Mozambique pa zifukwa zosadziwika.

Mkuluyu atamufunsa za anthuwo, akuti anauza apolisi kuti anawatenga m’boma la Mangochi, ndipo amapita nawo m’dzikolo kuti akawapezere ntchito.

Mulandu wa mkulu-yu unalowa m’bwalo pa 5 December 2017, ndipo First Grade Magistrate Ranwell Mangazi, ndi amene wapereka chigamulochi .

Elias Jafali amachokera m`mudzi mwa Ntonde m’dera la mfumu yayikulu Chowe m’boma la Mangochi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>