Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bwalo la Milandu Lilamula Anthu Asanu Kulipira 795,000 Kwacha

$
0
0

Bwalo lachiwiri la milandu m’boma la Machinga  lalamula amuna asanu ndi m’modzi 6 kuti alipire chindapusa cha ndalama zokwana 795,000 kwacha kulephera apo akakhale ku ndende kwa zaka zitatu atapezeka olakwa pa mlandu wakupha nsomba malo osayenera.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali, Constable Davie Sulumba, wati wapolisi wotengera nkhani ku bwalo la milandu Sub Inspector Rodrick Kamuona  anauza bwaloli kuti achitetezo anapeza amunawa akupha msomba mmbali mwa mtsinje wa Shire pogwiritsa ntchito ukonde, bwato komanso mbedza.

Anthuwa ati analandidwa zipangizozi ndi kumangidwa ndipo anawatsekulira mlandu wolowa kumalo osaloredwa, kugwiritsa ntchito zida zoletsedwa komanso kupha nsomba  m’malo otetezedwa.

Sub Inspector Kamuona anapempha bwaloli kuti liwapatse anthuwa chilango chokhwima kaamba koti mchitidwewu ati ukuchulukira mderali ndipo anthu ambiri akhala akumangidwa koma palibe chimene chikusintha.

Amunawa anapempha bwaloli kuti liwapatse chilango chofewerako kaamba koti ali ndi mabanja amene amawasamalira.

Popereka chigamulo chake Second Grade Magistrate Maxwell Boazi analumikizana ndi otengera nkhani ku bwalo la milanduyi ndipo analamula amuna asanu  kuti apereke 50,000kwacha aliyense pa mlandu uliwonse yomwe ndi 150,000 kwacha munthu aliyense ndipo wina anamulamula kuti alipire 45,000 kwacha pa milandu yonse.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>