Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Zipani Zotsutsa Zidzudzula ma Bank, MRA

$
0
0

Zipani zotsutsa boma m’dziko muno zati zipitiliza ndi ganizo lokakamiza boma kuti lidziunika ndondomeko zomwe ma Bank komanso bungwe lotolera misonkho m’dziko muno la Malawi Revenue Authority (MRA)amatsatira pa nkhani za chuma mdziko muno.

Poyankhula ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Blantyre,President wa chipani cha Peoples Progressive Movement(PPM) aMark Katsonga Phiri,wati zimenezi  zingathandize kuti boma likonze mfundo zabwino zokwezera ntchito za chuma pakati pa anthu ochita business zing’onozing’ono m’dziko  muno.

Iwo ati mfundo zomwe ma bank ndi bungwe lotolera misonkho laMRAlimatsatira zimakhala za nkhanza zomwe zimasonyeza kuti amakhala ndi cholinga chongofuna kupeza phindu lochuluka posaganizira aMalawim’dziko muno.

Polankhulanso president wa chipani cha New Labour a Sam Mpaso wati naye akugwilizana ndi zina mwa mfundo zomwe mtsogoleri wa chipani cha PPM a Katsongaanena ndipo wati akanakonda patakhazikitsidwa bungwe lapadera lowunika momwe bungwe la MRA limagwilira ntchito zake.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>