Mwambo wa chaka cha utumiki wa ana mu dayosizi ya Mangochiwachitikaku parishyaKochemu dayosizi-yi.
Malingana ndi mkulu wowona za utumiki wa ana mu dayosizi-yi, mwambo-wu unayamba ndi mwambo wa nsembe ya misa yomwe anatsogolera ndi episikopiwa dayosiziyi AmbuyeMontfort Stima.
Iwo alimbikitsa ana omwe anafika kumwambowu kuti apitilize kudzipereka mu mpingo.
Ana ochokera m’ma parish onse opezeka mu dayosizi-yi, ndi omwe afika ku mwambo-wu.
Mwambo wa chikondwelero cha utumiki wa ana mdziko muno udzafika pachimake penipeni pa 7 January 2018, pomwe mpingo wakatolika m’dziko muno udzakhale ukugwilizana ndi mpingo-wu pa dziko lonse kuchita mwambo wa chaka cha epifania, chomwe ndi cha utumiki wa ana.