Bwalo lachiwiri la milandu m’boma la Mangochi, lalamula amuna awiri kuti akakhale kundende ndi kukagwira ntchito yakalavulagaga kwa zaka zinayikaamba kopezeka ndi mulandu wakuba mbuzi.
Wapolisi wotengera nkhani ku bwalo la milandu, Constable Augastine Kagwira, anauza bwalolo kuti amuna-wa, Grecian Sikelo wa zaka 48 zakubadwa, komanso Andiwochi Ingresi wa zaka 57 zakubadwa anapalamula mulanduwu 23 November 2017 pomwe anakathyola khola la a Mariam Ayatu, a m’mudzi mwa Chaponda, m’dera la Sub T/A Namabvi m’bomalo, ndi kuwabamo mbuzi zisanu ndi zinayi(9), zomwe zandalama zokwanira 180 Thousand Kwacha.
Zitangochitika izi mayiwa anakapeleka lipoti kwa apolisi aku Namalaka, omwe anasakasaka ndi kugwira anthuwo.
Popeleka chigamulo chake Second Grade Magistrate, Augastine Mizaya, anati zomwe amuna wa anachita zinali zosayenera ndipo anawapatsa chilango chokhwimachi kuti ena atengeropo phunziro.
AGrecian Sikelo amachokera m’mudzi mwa Kantandiwo mdera la mfumu yayikulu Masaka m’boma la Ntcheu, pomwe a Andiwochi Ingresi,amachokeram’mudzi mwaTumbwem’dera la aSub T/A Namabvi,m’boma laMangochi.