Radio Maria Malawiati yakonza ndondomeko zosiyanasiyana pofuna kupititsa patsogolo ntchito za wailesiyi ndi cholinga choti itumikire bwino omvera ake mchaka cha 2017.
Mkulu woyendetsa mapologalamuku wailesiyi Bambo Joseph Kimu ndi omwe anena izi pambuyo pa msonkhano omwe mavolontiya komanso akuluakulu a wailesiyi anali nawo ku St. Louis Montfort parish m’boma laBalaka.
Iwo ati wailesiyi ipitiriza kuwapatsira omvera ake mapologalamu okoma mchakachi komanso ati akufuna kubwenza ngongole yomwe wailesiyi ili nayo yomwe ndi yoposa 50 millionkwacha.