Bambo wina wa zaka 47zakubadwawadzipha podzimangilira m’boma la Dedza.
Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Edward Kabango, bambo-yu ndi Ives Kumankhamba ndipo anali mphunzitsi pa sukulu ya pulayimale ya Buam’bomalo.
Malemuyi akuti wadzipha mkazi wake anali kumudzi komwe amakazonda odwala. Padakalipano gwero la imfa ya mkulu-yi silikudziwika.
Malemu Ivesi Kumankhamba amachokera m’mudzi mwa Fosa kwa mfumu yaikulu Kachere m’boma lomwelo la Dedza.