Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha anthu kuti apemphelere anthu a mdera la Rohingya mdziko la Myanmar omwe akuphedwa komanso kukakamizidwa kuti achoke mnyumba zao.
Papa amalankhula izi lachitatu ku likulu la mpingowu ku Vatican pa mkumano omwe amakhala nawo ndi anthu osiyanasiyana omwe amakayendera likulu la mpingo wakatolikali.
Iye wati kwa nthawi yaitali anthuwa akhala akuphedwa ngakhalenso kuzunzidwa kumene kaamba ka chikhulupiliro chomwe ali nacho mu chipembedzo chao cha chisilamu.
Padakali pano mabungwe omenyera maufulu a anthu apempha boma la dziko la Myanmar kuti lipeze gulu loyima palokha kuti lichite kafukufuku wa zomwe zikuchitika mdzikolo.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati anthu pafupifupi 1 miliyoni mdzikolo amasalidwa kamba ka chipembedzo chao cha chi Budda kaamba koti ambiri mwa iwo anathawa mdziko la Bangladesh, ndipo akukhala mdziko la Myanmar opanda zowayenereza.