Anthu pafupifupi 37 afa ndipo ena oposera 70 avulala kaamba ka moto omwe unabuka pa chipatala china cha Sejong mdziko la South Korea.
Pa nthawi yomwe motowu umayamba kubuka, mu chipatalachi munali anthu pafupifupi 2 hundred ndipo akuwuganizira kuti unayambira mu chipinda chomwe anthu odwalitsitsa amafikira.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBCmagulu ozimitsa moto ati anthu omwe amwalira pa ngoziyi, afa kaamba koti anabanika ndi utsi wa motowu.
Malipoti ati padutsa zaka khumi, ngozi ya moto wa mtunduwu chichitikireni mdzikolo ndipo pali chiyembekezo chakuti chiwerengero cha anthu omwalirawa chitha kukwera kaamba koti ambiri mwa anthu omwe avulala, avulala modetsa nkhawa.