Dziko laMalawimawa ligwilizana ndi mayiko pa dziko lonse pochita mwambo wa tsiku loganizira nyumba zoulutsira mawu padziko lonse (World Radio Day).
Mwambo wa ukulu woganizira tsikuli unachitikira ku Monkebay m’boma la Mangochi pa mutu woti “Wailesi ndi Masewero” maka poyang’ana masewero omwe amatengedwa ngati osafunikira kwenikweni.
Bungwe lopeleka ziphatso za wailesi m’dziko muno la Malawi Communication Reguratory Authority (MACRA)ndi lomwe lakonza mwambowu ndi thandizo kuchokera ku bungwe la UNESCO.
Pokonzekera tsikuli bungweli linakonza maphunziro a tsiku limodzi a atolankhani ochokera mu nyumba zing’onozing’ono zoulutsira mawu m’boma la Mangochi komwe mwa zina lathandiza atolankhani a mu nyumbazi za udindo umene ali nawo pa ntchito zokweza masewero osiyanasiyana omwe amachitika mdziko muno kudzera pa wailesi.
Maphunziro-wa anachitikira kuDzimwe Community Radio m’bomalo.