Mayi wina wafa khoma la nyumba litamugwera m’boma laNtchisi.
Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi m’bomaloSergeantGladson Mbumpha,malemu mayiMelina Felix akuti khudzidwa ndi imfayi pa nthawi imene amagwetsa zipupa za nyumbayo kuti ikonzedweso.
Malingana ndi a M’bumpha nyumba ya mayiyu yemwe anali wa chikulire akuti sinali bwino, ndipo imayenera kugwetsedwa, ndipo pa 11 February 2018 ndi pomwe mayiyu anayamba kugwetsa nyumbayo, mwatsoka khoma la nyumbayo linawagwera, ndipo anthu atafika kuti adzapulumutse, anapeza kuti mayiko wafera pomwepo, ndipo achipatala atsimikizanso za imfa ya gogo-yu.
Malemu mayiMelina Felixanali a zaka82zakubadwa ndipoamachokera m’mudzi mwa Phale m’dera la mfumu yayikuluChilookom’bomalo lomwelo la Ntchisi.