Akiepisikopi wa Akidayosizi ya Lilongwe ya mpingo wakatolika Ambuye Tarcizius Ziyaye apempha akhristu kuti alimbikitse ndi kupempherera anzawo omwe akupikisana nawo pa chisankho cha pa 20 May ponena kuti ndale sichinthu choipa.
Ambuye Ziyaye ayankhula izi lachiwiri ku Maula Cathedral mumzinda wa Lilongwe pamwambo wa msembe ya misa wodalitsa mafuta oyera komanso chaka cha ansembe.
Pa mwambowu Episkopi amadalitsa mafuta oyera omwe mwa zina mpingo umawagwiritsa ntchito pozozela odwala komanso popereka masacramenti a ubatizo ndi ulimbitso.
Ambuye Ziyaye ati ndikofunika kuti akhristu omwe akupikitsana nawo ngati makhansala, aphungu akunyumba ya malamulo komanso pulezidenti pa chisankho chapatatu cha chikudzachi alimbikitsidwe kuti choncho akadzapambana adzathe kutumikira anthu potsata chifuniro cha Mulungu.
“Akhristu ena ofuna kuti atumikire m’boma tiziwathandiza kuti kutumikirako akhaledi nyale yowunikira dziko lapansi pano chifukwa nkotheka ndithu kugwira bwinobwino ntchito imeneyi. Sintchito yoyipa ayi koma mowongoleledwa ndi thandizo la Mulungu.“Iwo anatero.
Ambuye Ziyaye alangiza akhristu kuti adziwerenga kalata yomwe Aepiskopi a mdziko muno anatulutsa miyezi yapitayo chifukwa ndiyomwe ingawathandize kudzasankha atsogoleri oyenera pachisankhochi.
“Inu akhristu eni ake kalata ija ya Aepiskopi tiziyisinkhasinkha chifukwa imatiwunikira kuti tizasankhe bwinobwino powonongoleledwa. Kalata imene ija sikuti ife a episkopi ndi mawu athu koma mukawona muli mawo a Mulungu, zogwirizananso ndi zachilungamo ndi mtendere.” Anatero Ambuye Ziyaye.