Cardinal John Njue wafika ku Malawi kuzakhala nawo pa msonkhano wa nambala 18 wa bungwe la atsogoleri ampingo wakatolika m’maiko amchigawo cha AMECEA omwe ukuyamba pa 16 july mpaka 26 July ku Bingu International Conference Center mumzinda wa Lilongwe.
Cardinal Njue yemwe ndi membala wamkulu wa board ya AMECEA anafikira ku bwalo la Kamuzu International mumzinda wa Lilongwe lolemba komwe analandiridwa ndi wachiwiri kwa pulezidenti wadziko lino a Saulos Chilima, Archepiskopi Tarsizius Ziyaye wa archdayosizi ya Lilongwe yemwenso ndi wapampando wa bungwe la AMECEA kuzanso mlembi wamkulu wa bungwe la AMECEA bambo Ferdinand Lugunzo.
Poyankhula kwa atolankhani atangofika ku bwalo la ndegelo, Cardinal Njue anayamikira boma la Malawi chifukwa chomulandira bwino ndipo anati misonkhano ya bungweli ndiyofunikira kwambiri ku mpingowu.
M’mawu awo, Ambuye Ziyaye anati dziko la Malawi limadziwika kuti ndi la anthu owopa Mulungu ndipo anati ino ndi nthawi yoyenera kutsimikizira zimenezi kudzera mmaanja athu.
“Mpingo wa katolika ukuyenera kusintha posiya kudalira thandizo la azungu pogwira ntchito modzipereka popeza njira zina zopezera ndalama pawokha” anatero Ambuye Ziyaye.
Bungwe la Association of Member Episcopal Conferences in Eastern Africa (AMECEA) ndilopangidwa ndi maiko a Malawi, Kenya, Sudan, Tanzania, Eritrea, Zambia, Uganda ndi Ethiopia.
Msonkhano wa AMECEA umachitika zaka zitatu zilizonse ndipo aka kakhala kachitatu dziko la Malawi kuchititsa msonkhanowu.