Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Beam Trust Yakonzeka Kulimbikitsa Amayi pa Chuma

$
0
0

Bungwe la Beautify Malawi (BEAM) TRUST lati posachedwapa liyamba kulimbikitsa amayi komanso asungwana kukhala odzidalira pachuma pamwamba pa ntchito zake zowonetsetsa kuti mdziko muno muli ukhondo.

Mkulu wa bungweli Mayi Getrude Hendrina Mutharika,yemwenso ndi mayi wa fuko la dziko la Malawi, ndi yemwe wanena izi kulikulu la bungwe la United Nations mumzinda wa New York mdziko la America, pamwambo okhazikitsa tsiku lodzidalira pachuma padziko lonse.

Iye anati bungweli lizigwiritsa ntchito zinyalala zomwe lizitolera mdziko muno pozisandutsa zinthu zomwe zingathandize amayi komanso asungwana kupeza chuma, chomwenso chingathandize kupititsa patsogolo chitukuko cha dziko Malawi.

Mayi Mutharika anauza nthumwi ku msonkhanowo kuti kusowa kwa chikole, Matenda a Malungo, komanso HIV ndi Edzi ndi ena mwamavuto omwe amayi ndi asungwana akukumana nawo mu Africa, ngakhalenso mdziko la Malawi.

Pamenepa iwo apempha mabungwe ndi makampani kuti agwirane manja ndi mabungwe ngati Beam pa ntchito yolimbikitsa amayi kukhala wodzidalira pa chuma.

Mayi wa fukoyu watsimikiza kuti bungwe lake lichita chotheka kuti cholinga chake chowonetsetsa kuti mdziko la Malawi  muli ukhondo chikwanilitsidwe, pofuna kuthandizanso amayi kuchita malonda awo mmalo osamalilika.

Mwambowu womwe unachitika ndi mutu wakuti "Amayi Odzidalira ndi Makina Atsopano Opititsira Patsogolo Chitukuko cha Makampani Mmaiko Amene Akukwera Kumene," panafika amayi omwe anachita bwino pa ntchito zamalonda, mabungwe omwe si aboma ndi magulu osiyanasiyana.

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>