Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

MAGANIZO A ANTHU PA ZA KUPUMA UDINDO WA APAPA

$
0
0


 

Pamene anthu akupitiliza kuthilirapo ndemanga pa ganizo la mtsogoleri wa Mpingo wa
Katolika pa dziko lonse, Papa Benedikito wachi 16 lopuma pa udindowu mwezi uno,
anthu mdziko muno ayamikira papayu chifukwa cha ganizoli.

Anthuwa apereka kuthokoza kwawo kudzera palamya pambuyo pa pulogalamu yapadera yomwe radio
Maria Malawi inaulutsa yofotokoza zomwe zimachitika pofuna kusankha papa
watsopano.

Ambiri mwa anthuwo ayamikira Papa Benedikito wachi 16 chifukwa chozindikira kufooka
kwa umoyo wake wa thupi chifukwa choti wakula ,zomwe anthuwa akuti ndi zosowa
mwa atsogoleri ambiri omwe amakhala m’maudindo osiyanasiyana.

“Ife tikuyamika kwambiri zomwe papayu wachita ndipo ichi ndi chitsanzo chabwino
kamba koti atsogoleri ambiri amakakamira maudindo awo ngakhale atakula
kwambiri”, m’modzi mwa anthu omwe analowa nawo mu pologalamuyi.

 

Mkulu woona za ma pulogalamu ku wailesiyi, Bambo Joseph Kimu ati  wailesiyi ipitiliza kulongosolera anthu zomwe zidzichitika pa nthawiyi.

 

Pakadali pano Mpingo wa Katolika kuno ku Malawi watsimikizira anthu kuti akhala akudziwitsidwa
zonse zimene likulu la Mpingowu ku Vatikani likhale likulengeza pamene
mtsogoleri wa Mpingowu akhale akupuma paudindowu kumathero a mwezi uno.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>