Nthenda ya khansa ya mchiberekero akuti ndi imodzi mwa matenda omwe akupitilira kutenga miyoyo ya amayi kamba koti amayi ambiri samapita kukayezetsa kuti adziwe ngati ali ndi matendawa kapena ayi.
Mmodzi mwa akatswiri ophunzitsa anamwino mdziko muno Professor Address Malata, yemwenso ndi mkulu wa sukulu ya anamwino ya Kamuzu College of Nursing KCN,ndi yemwe wanena izi polankhula ndi mtolankhani wathu mu mzinda wa Blantyre pambuyo pa sabata imodzi yoganizira matendawa yomwe inachitika posachedwapa.
Professor Malata awuza Radio Maria Malawi kuti nthendayi ndi yochizika koma imafunika idzwike msanga isadafike poyipa.
Iwo ati amayi ambiri amamwalira ndi matendawa kamba kosowa ndalama zopitira kunja kukalandira thandizo la matendawa kamba koti pamafunika ndalama zochuluka.
“Amayi ambiri amene amamwalira mdziko muno amamwalira ndi khansa ya khomo la chiberekero zomwe dziko la Malawi likufunika kutengapo gawo poteteza amayiwa,” anatero a Malata.
Pamenepa mayi Malata apempha atsikana kuti asamayambe kugona ndi amuna ali achichepere kamba koti ali pa chiopsezo chopezeka ndi matendawa.
Masiku apitawa chipatala cha Mwayiwathu chinali pa dongosolo loyesa amayi ngati ali ndi matendawa mwa ulere.
Polankhula mmodzi mwa madotolo pa chipatalapo Dr Bonus Makanani ati izi zathandiza amayi ambiri kudziwa mmene alili,ndipo amene apezeka ndi nthendayi awauza chochita.
Dr Makanani ati, “amayi amene apezeka ndi matendawa ali ndi mwayi wolandira thandizo ngati angakwanitse, koma enawo tawatumiza ku chipatala chachikulu cha QUECH kuti akalandire thandizo.”
Matenda a khansa ya khomo la chiberekero akupezeka ndi amayi a mmayiko amene akukwera kamba koti amayi sakhala ndi chidwi chokayezetsa matendawa.