Unduna wowona za ntchito m’dziko muno wapempha anthu ogwira ntchito m’boma kuti adzitsatira malamulo akafuna kunyanyala ntchito pamavuto omwe akukumana nawo.
Nduna mu undunawu wolemekezeka a Henry Mussa, ndi yomwe yapereka pempholi lachitatu pa msonkhano wa atolankhani omwe unachitikira mumzinda wa Lilongwe.
Ndunayi inayitanitsa msonkhanowu pamene anthu ogwira ntchito mmadipatimenti osiyanasiyana a boma akupitiliza kunyanyala ntchito pofuna kukakamiza boma kuti liwakwezere malipiro, pomwe ena akudandaula kuti sadalandire malipiro awo a miyezi yapitayi.
A Mussa ati mkulakwa kuti anthu ogwira ntchito za boma, azinyanyala ntchito zawo mosatsatira malamulo,ndipo apempha anthuwa kuti adzidziwitsa undunawu pasanathe sabata imodzi ngati pali cholakwika pa ntchito yawo.
Iwo apempha anthu kuti ngati akukumana ndi mavuto pa ntchito yawo akuyenera kudziwitsa unduna wawo pasanathe masiku asanu ndi awiri asanapange ganizo lonyanyala ntchito, pofuna kuti azikhala ndi nthawi yokonza dongosolo pokonza mavutowo.
Pamenepa a Mussa ati mchitidwe wonyanyala ntchito womwe wakula kwambiri mdziko muno anthu adziwe kuti chitukuko cha dziko lino sichingapite patsogolo.
Padakali pano undunawu uwonetsetsa kuti anthu ogwira ntchito m’boma komanso mmakampani azilandira chisamaliro chokwanira.