Wachiwiri kwa mkulu woyang’anira ma pulogalamu ku Radio Maria Malawi Bambo Charles Kaponya wayamikira akhristu kamba ka chidwi chawo potenga gawo lothandiza wailesiyi.
Bambo Kaponya amalankhula izi pambuyo pa mwambo wa nsembe ya misa womwe unachitika lamulungu pa 30 November 2014 ku Ntcheu Parish mu dayosizi ya Dedza, womwe cholinga chake chinali chofuna kupeza thandizo lothandizira wayilesiyi.
Iwo analimbikitsa akhristu kuti apitilize kuthandiza wailesiyi kuti cholinga chake chipitilire kupita patsogolo.
Pamwambowu panapezeka ndalama zokwana 3 hundred and 35 thousand kwacha, matumba 7 achimanga ndi katundu wina osiyanasiyana.
Mwambo ngati womwewu unachitikanso ku St Pius Parish mu Arki Dayosizi ya Blantyre, polankhula Bambo Mfumu wa Parishiyi Bambo Benito Masuwa anayamikira abwenzi ndi anthu onse kamba ka thandizo limene anapereka, ndipo pa mwambowu panapezeka ndalama zokwana 4 hundred and 19 thousand kwacha, komanso matumba awiri a chimanga.