Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

ALAMULIDWA KUKAKHALA KU NDENDE ZAKA ZINAYI KAMBA KOBAYA MUNTHU

$
0
0

 

Bwalo la milandu la magistrate m’boma la Dowa lalamula mwamuna wina kuti wa kumalo osungira anthu othawa kwawo a Dzaleka kuti akakhale kundende zaka zinayi kamba kovulaza mnyamata wina wa zaka 16 pomubaya ndi mpeni.

Mneneli wa apolisi ku Dowa  a Richard Kaponda atsimikizira   Radio Maria ndipo ati mwamunayo a Selastine Hachizama a zaka 37 omwe kwao ndi ku Bubanza m’dziko la Burundi adabaya Elberto Isaac pa12 february 2013 ati pomuganizira kuti adali wakuba.

“A Hachizama adabaya nyamatayo panthawi yomwe ankadutsa pafupi ndi nyumba yawo  pa 10 February cha m’ma 1 koloko m’bandakucha. Panthawiyo Isaac yemwe kwawonso ndi ku Burundi, amachokera kumalo ena owonetsera kanema kupita kunyumba kwawo podutsira kunyumba kwa mkuluyo. Atamva
kuti panja pa nyumba yao pakudutsa munthu a Hachizama adatuluka panja ndi kubaya nyamatayo ndi mpeni pachifuwa kawiri ati pomuganizira kuti adali wakuba. Anthu ozungulira malowo akuti adafika pa malowo kuti akathandize mkuluyo kulanga mbavayo koma atazindikira kuti nyamatayo sanali wakuba  anthuwa anakatula nkhaniyi kupolisi omwe adamanga a Hachizama”, watero Kaponda.

Popereka chigamulo First Grade Magistrate Titus Banda walamula mkuluyo kuti akakhale kundende ndikugwira ntchito yakalavula gaga kwa zaka zinayi kuti anthu ena atengerepo phunziro.

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>