M’bindikiro wa sabata imodzi wa ansembe a chibadwiri mudayosizi ya Mangochi utha mawa.
M’bindikirowu unayamba lolemba sabata ino ndipo ukuchitika pofuna kukonzekera kubadwa kwa Yesu Khristu, kuti nawo athe kukonzekeretsa akhristu mumpingowu muuzimu komanso mthupi munyengoyi.
Polankhula ndi mtolankhani wathu mkulu wowona zautumiki wamumpingowu mu Arkdayosizi ya Blantyre Bambo Alfred Chaima ndi omwe anena izi dzulo pambindikiro wa ansembe a chibadwiri a mudayosiziyi ,omwe iwo akutsogolera ku Montfort House ku Namiyasi mboma la Mangochi.
Bambo Chaima ati ansembe, amagwira ntchito imene Yesu Khristu mwini anayisiya, choncho akuyenera kumapeza nthawi yapadera yosinkhasinkha za moyo wawo ngati atumiki maka kumapeto a chaka pofuna kuwona momwe utumiki wawo wayendera muchakachimenecho. A episcope a Diocese ya Mangochi Ambuye Montfort Sitima akuchita nawo m’bindikirowu.