Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ntchito za Kusamalira a Mndende Zayenda Bwino mu Chaka cha 2014

$
0
0

Nthambi yoyang’anira chisamaliro cha anthu ku ndende mu ark-dayosizi ya Blantyre yati ndiyokhutira ndi momwe ntchito zake zayendera mchaka cha 2014.

Bambo mlangizi oyang’anira nthambiyi mu ark-dayosiziyo Bambo Chisiano  Lawrenti ndi omwe anena izi lamulungu pamene nthambiyi inakayendera anthu omwe akusungidwa ku ndende ya Chichiri mu mzinda wa Blantyre.

Bambo Lawrenti ati nthambiyi imachiwona chofunika kwambiri kusamalira anthu akundende kamba koti ntchito yosintha makhalidwe a anthu kudzera mu ntchito za ndende, siyingatheke ndi thandizo la boma lokha.

Iwo ati nchifukwa chake nthambiyi yakhala chaka chonsechi ikuyendera komanso kusamalira anthu omwe ali kundende maka za Chichiri ndi Bvumbwe pofuna kuthandiza boma kusamalira komanso kusintha makhalidwe a anthuwa.

Sister Anna Tomas a chipani cha Francisco Woyera, omwe amatumikira limodzi ndi Bambo Lawrenti maka popereka upangiri, maphunziro komanso chisamaliro kwa anthu omwe ali kundende mu arkdayosiziyo ndinso ndende zina ati iwo amayesetsa kuti azipereka thandizo  maka kwa odwala pofuna kuti a mndende ambiri asamataye moyo wawo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>