Episkopi wa Arch-diocese ya Lilongwe olemekezeka ambuye Tarcizio Ziyaye wati mchitidwe umene mayiko olemera akumachita polimbikitsa maukwati a pakati pa amuna kapena akazi okhaokha ndi amene akusokoneza tsogolo la mabanja.
Ambuye Ziyaye alankhula izi kwa akhristu a mpingowu amene anasonkhana ku parish ya Msamba mu Arch-diocese-yo kuchita Chaka cha Banja Loyera la Yosefe, Maria ndi mwana wawo Yesu .
Iwo ati akhristu akuyenera kuonetsetsa kuti sakukopeka ndi mchitidwewu, koma kulimbikitsa mabanja a pakati pa mwamuna ndi mkazi kamba koti awa ndiwo mabanja ovomelezeka pamaso pa Mulungu.
Pamenepa iwo anayamikira mtsogoleri wa mpingo wakatoloka pa dziko lonse Papa Francisco kamba ka chilimbikitso chomwe wakhala akupereka kuti moyo wa mabanja uzame komanso kuti akhristu asabwelere mmbuyo.