Chiwerengero cha ansembe ndi atumiki ena a mpingo wa katolika omwe akhala akuphedwa akuti chakwera kwambiri mdziko la Mexico.
Malinga ndi zotsatira za kafukufuku amene bungwe la Catholic Multimedia Center for the Mexican Bishops Conference lachita m’dzikomo, kafukufukuyi waonetsa kutim’chaka cha 1990 kufikira chaka cha 2014, atumuki ambiri ogwira ntchito zotumikira mpingo wakatolika m’dzikomo , monga ansembe ndi atumiki ena akhala akuphedwa ndi kuchitilidwa ziwembu zosiyanasiyana m’dzikomo .
Bungweli lati magulu a zigawenga zochita malonda ogulitsa makhwala ozunguza bongo, ndi omwe akhala akudzudzulidwa kuti ndi omwe akhala akulimbikitsa zichiwembuzi, ati podana ndi mauthenga owadzudzula amene atumiki a mpingowu akhala akufalitsa mdzikomo.