Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Dayosizi ya Mangochi Yati Ana Akuyenera Kuyikidwa Patsogolo mu Nkhani Za Mpingo

$
0
0

Episkopi wa Dayosizi ya Mangochi Ambuye Montfort Sitima ati ana akuyenera kuyikidwa patsogolo pankhani zokhudza mpingo.

Ambuye Sitima alankhula izi lachitatu pa msonkhano wa mabungwe a ana otumikira mumpingowu omwe unachitikira ku Mangochi Cathedral mudayosiziyi.

Iwo ati zambiri zomwe zimakambidwa mumpingo kuphatikizapo ulaliki, zimakhala zokhudza akuluakulu,ndipo ati mpofunika kuti ana adziyikidwa patsogolo maka powakonzera zochitika zawo pomwe azitha kuthandizana pa zosowa zawo za thupi komanso uzimu.

Polankhulapo mkulu wowona zautumwi wa mabungwe  a Papa kulikulu la mpingo wakatolika mdziko muno Bambo Vincent Mwakhwawa ,alimbikitsa madayosizi onse a mpingowu mdziko muno kuti azikhala ndi tsiku lapadera chaka chili chonse lopereka mwayi kwa ana kuti azikumana malo amodzi pofuna kuti azithandizana pa nkhani za uzimu komanso thupi.

Iwo apereka pempholi pamene mpingowu Lamulungu  pa 4 January  likuyembekezeka kukhala likuganizira za utumiki wa ana womwe chaka chino mutu wake ndi ana kutumikira ana anzawo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>